2 Chronicles 6:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kumwamba kukatsekeka, mvula nkupanda kugwa, chifukwa chakuti anthuwo adakuchimwirani, pambuyo pake nkupemphera choyang'ana ku malo ano ndi kutamanda dzina lanu, natembenuka nkusiya tchimo laolo Inu mukuŵazunza,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukatsekeka m'mwamba, mopanda mvula, chifukwa cha kukuchimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene kumwamba kwatsekeka ndipo mvula sikugwa chifukwa anthu anu akuchimwirani, ndipo pamene apemphera akuyangʼana malo ano ndi kuvomereza Dzina lanu ndi kutembenuka kuchoka ku machimo awo chifukwa inu mwawalanga,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukatsekeka m'mwamba, mopanda mvula, cifukwa ca kukucimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa;