2 Chronicles 6:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Inuyo mumve kumwambako, mukhululukire tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisraele. Inu muziŵaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo, ndipo muzigwetsa mvula pa dziko lanu limene mudapatsa anthu anu kuti likhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israele, mutawalangiza njira yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera, ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire chimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israyeli, mutawalangiza njira, yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale colowa cao.