2 Chronicles 6:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwina mwake m'dzikomo mudzaloŵa njala, mliri, dzimbiri lapambeu kapena chinoni, dzombe kapena kapuchi. Mwina adani ao adzaŵazinga ku mzinda wao wina uliwonse. Mwina padzakhala mliri wamtundu wina kapena matenda a mtundu uliwonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la midzi yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene adani azungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala cinsikwi, kapena cinoni, dzombe, kapena kapuce; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la midzi yao; mukakhala mliri uli wonse, kapena nthenda iri yonse;