2 Chronicles 6:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Inuyo mumve kumwambako kumene mumakhala. Mukhululuke ndipo muchitepo kanthu. Muchitire aliyense potsata makhalidwe ake onse pakuti Inu mukudziŵa mtima wake. Inu nokha ndinu amene mumadziŵa mitima ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mumvere m'Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita popeza Inu mumadziwa mtima wake, (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu),
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mumvere m'Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera ali yense monga mwa njira zace zonse, monga mudziwa mtima wace; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;