2 Chronicles 6:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chimodzimodzinso mwina mlendo amene sali mmodzi wa Aisraele anthu anu, adzabwera kuchokera ku dziko lakutali, atamva za dzina lanu lotchuka ndiponso dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu. Iyeyo akadzabwera kudzapemphera ku Nyumba ino,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israele, akafumira ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono ndi kupemphera kuloza kunyumba iyi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo kunena za mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisraeli, koma wabwera kuchokera ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lotchukali, ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu, kudzapemphera akuyangʼana Nyumba ino,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israyeli, akafumira ku dziko lakutari cifukwa ca dzina lanu lalikuru, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono wanu wotambasuka; akadza iwowa ndi kupemphera kuloza ku nyumba iyi;