2 Chronicles 6:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mumchite mlendoyo zonse zimene wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu onse a pa dziko lapansi adziŵe dzina lanu, ndipo azikumverani monga m'mene amachitira Aisraele anthu anu, ndipo adziŵe kuti Nyumba imene ndaimangayi imadziŵika ndi dzina lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, nimumchitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisraele; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi itchedwa ndi dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi dzina lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, nimumcitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisrayeli; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi ichedwa ndi dzina lanu.