2 Chronicles 6:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono, ali akapolo kuchilendoko akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko laukapololo nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu,’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita choipa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati asintha mitima yawo ku dziko limene ali akapolo ndi kulapa ndi kukudandaulirani inu mʼdziko la ukapolo wawo ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa ndipo tachita moyipa kwambiri.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tacimwa, tacita mphulupulu, tacita coipa;