2 Chronicles 6:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
anthuwo akabwerera kwa Inu ndi maganizo ao onse ndi mtima wao wonse, m'dziko laukapolo kumene iwo aja adaŵatengera, ndipo akapemphera choloza ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m'dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mudzi mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati atembenukira kwa inu ndi mtima ndi moyo wawo wonse mʼdziko lawo la ukapolo kumene anatengedwako ndi kupemphera moyangʼana dziko limene inu munalipereka kwa makolo awo, moyangʼana Nyumba yanu imene ndakumangirani;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika