2 Chronicles 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangemo nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Ndipo sindidasankhepo munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira Aisraele anthu anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankha mudzi uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba kuti ndizikhalamo kapena munthu wina aliyense kuti akhale mtsogoleri wa Aisraeli anthu anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse m'mafuko onse a Israyeli, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu ali yense akhale kalonga wa anthu anga Israyeli;