2 Chronicles 7:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiŵiriwo, Solomoni adauza anthu aja kuti apite kwao. Anthuwo anali okondwa ndiponso a mtima wosangalala, chifukwa cha zokoma zimene Chauta adaachitira Davide ndi Solomoni ndiponso Aisraele, anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku la makumi awiri ndi chitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao chifukwa cha zokoma Yehova adawachitira Davide, ndi Solomoni, ndi Aisraele anthu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku la makumi awiri ndi citatu la mwezi wacisanu ndi ciwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao cifukwa ca zokoma Yehova adawacitira Davide, ndi Solomo, ndi Aisrayeli anthu ace.