2 Chronicles 7:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Solomoni adamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu ndipo zonse zimene adaaganiza kuti achite m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba yake adazimalizadi mokhoza kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Solomoni anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo zilizonse zidalowa mumtima mwake mwa Solomoni kuzichita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yakeyake, anachita mosalakwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene zinali mu mtima mwake pa Nyumba ya Yehova ndi nyumba yake yaufumu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Solomo anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo ziri zonse zidalowa mumtima mwace mwa Solomo kuzicita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yace yace, anacita mosabwezeza.