2 Chronicles 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ukatero Ine ndidzaukhazikitsa mpando wako waufumu, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu, monga ndinachitira pangano ndi abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu wolamulira Israeli.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu m'Israyeli.