2 Chronicles 7:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Nyumba yotchuka ndi yokomayi, aliyense wopitapo adzadabwa nadzafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta walichita zotere dzikoli, ndiponso Nyumbayi?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yehova anatero ndi dziko lino ndi nyumba yino chifukwa ninji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yeliova ana tero ndi dziko lino ndi nyumba yino cifukwa ninji?