2 Chronicles 7:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aisraele onse ataona moto wotsika kumwambawo, pamodzi ndi ulemerero wa Chauta m'Nyumba ya Chauta ija, adaŵerama, nazyolikitsa nkhope zao pansi, ndipo adapembedza nathokoza Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova panyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse ataona moto ukuchokera kumwamba ndi ulemerero wa Yehova pamwamba pa Nyumba ya Mulungu, anagwada poyalidwa miyalapo ndipo anagunditsa nkhope zawo pansi, ndi kulambira ndi kutamanda Yehova, ponena kuti, “Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala chikhalire”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana onse a Israyeli anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova panyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire.