2 Chronicles 7:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe adaimirira m'malo mwao, pamene Alevi ankatamanda Chauta poimba nyimbo zothokoza Chauta ndi zipangizo zimene Davide adapanga, pakuti chikondi cha Mulungu chimakhala mpaka muyaya. Anthu onseŵa ankatero nthaŵi zonse Davide akamapereka matamando kudzera mwa iwo. Poyang'anana ndi iwowo panali ansembe oliza malipenga. Ndipo Aisraele onse adaakhala chilili.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naimirira ansembe m'udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naimirira ansembe m'udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoyimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala ciriri Israyeli yense.