2 Chronicles 7:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero cha masiku asanu ndi aŵiri pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha ku Hamati mpaka ku kamtsinje wa ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisraele onse pamodzi naye, khamu lalikulu ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero kwa masiku asanu ndi awiri pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku chigwa cha ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, khamu lalikuru ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Aigupto.