2 Chronicles 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adatenga mwana wamkazi wa Farao ku mzinda wa Davide, nabwera naye ku nyumba imene adamangira mkaziyo, poti Solomoniyo ankati, “Mkazi wanga asamakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele, chifukwa chakuti malo amene kwafikira Bokosi lachipangano la Chauta ngopatulika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israyeli; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.