2 Chronicles 8:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka potsata malamulo a Mose okhudza masiku a Sabata, masiku a pokhala mwezi watsopano, ndiponso masiku achikondwerero atatu a chaka ndi chaka: Chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, chikondwerero cha masabata ndiponso chikondwerero cha mahema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka, pa zikondwerero za Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa zikondwerero za Masabata, ndi pa zikondwerero za Misasa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka nsembezo potsata malamulo a Mose okhudza chikondwerero cha Masabata, chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndi zikondwerero zitatu za pa chaka: Chikondwerero cha Buledi Wopanda yisiti, Chikondwerero cha Masabata ndi Chikondwerero cha Misasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa madyerero oikika, katatu m'caka, pa madyerero ali mkate wopanda cotupitsa, ndi pa madyerero a masabata, ndi pa madyerero a misasa.