2 Chronicles 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potsata malangizo a Davide bambo wake, adagaŵa ansembe m'magulumagulu ndi kuŵapatsa ntchito zao. Adaikanso magulu a Alevi ndi kuŵapatsa ntchito yao yoimba nyimbo zotamanda Mulungu ndi yotumikira ansembe, monga momwe ntchito ya tsiku lililonse inkafunikira. Magulu a alonda apazipata adaŵagaŵira udindo wao pa chipata chilichonse. Paja Davide, munthu wa Mulungu, anali atalamula motero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potsata malangizo a Davide abambo ake, iye anayika ansembe mʼmagulumagulu monga mwa ntchito zawo ndipo anayika Alevi kukhala otsogolera matamando ndi kuthandiza ansembe pa zofunika pa tsiku lililonse. Iye anasankhanso magulumagulu a alonda a pa zipata zosiyanasiyana, chifukwa izi ndi zimene munthu wa Mulungu, Davide analamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika monga mwa ciweruzo ca Davide atate wace zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku cipata ciri conse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.