2 Chronicles 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Hiramu adamtumizira zombo ndi anyamata ake amene ankadziŵa za zapanyanja. Anthuwo adapita ku Ofiri, pamodzi ndi anyamata a Solomoni, ndipo adakatengako golide wa makilogramu 18,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amarinyero ace, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomo ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golidi, nabwera nao kwa Solomo mfumu.