2 Chronicles 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanganso Baalati ndiponso mizinda yonse yosungiramo zinthu zimene anali nazo, mizinda yonse yosungiramo magaleta ake, ndi ina yomakhalamo anthu ake okwera pa akavalo, ndi zonse zimene Solomoni adafuna kuti amange ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene Solomoni ankaŵalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Baalati, ndi midzi yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi midzi yonse ya magaleta ake, ndi midzi ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Balati, ndi midzi yonse yosungiramo cuma anali nayo Solomo, ndi midzi yonse ya magareta ace, ndi midzi ya apakavalo ace, ndi zonse anazifuna Solomo kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.