2 Chronicles 8:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aisraele Solomoni sankaŵagwiritsa ntchito yaukapolo. Iwowo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, oyang'anira magaleta ake ndi anthu ake okwera pa akavalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mwa ana a Israele Solomoni sanawayese akapolo omgwirira ntchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ake akulu, ndi akulu a magaleta ake, ndi apakavalo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Aisraeli; Iwo anali anthu ake ankhondo, atsogoleri a ankhondo, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mwa ana a Israyeli Solomo sanawayesa akapolo omgwirira nchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ace akuru, ndi akuru a magareta ace, ndi apakavalo ace.