2 Chronicles 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali. Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni, inabwera mu Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri, ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo, anadza kumuyesera Solomo ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukuru, ndi ngamila zosenza zonunkhira, ndi golidi wocuruka, ndi timiyala ta mtengo wace; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.