2 Chronicles 9:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mitengo ya mbawayo mfumu idasanjira makwerero a ku Nyumba ya Chauta ndi a ku nyumba ya mfumu. Ndipo anthu oimba nyimbo adaŵapangira apangwe ndi azeze, amene kunalibe nkale lonse ku dziko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya mʼbawa pokonzera makwerero a Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndiponso kupangira anthu oyimba apangwe ndi azeze. Zinthu zonga zimenezi sizinaonekeponso mu Yuda).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oyimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.