2 Chronicles 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu pafupi asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Solomoni inapanga zishango zazikulu 200 zagolide wosasantha. Mʼchishango chilichonse mumalowa golide wolemera makilogalamu asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Solomo anapanga zikopa mazana awiri za golidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinathera golidi wonsansantha masekeli mazana awiri.