2 Chronicles 9:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira makilogramu atatu. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide wosasantha ndipo chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu. Mfumu inayika zishangozi mʼnyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napanganso malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinathera masekeli mazana atatu a golidi; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.