2 Chronicles 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndiponso chopondapo mapazi, zonsezo zagolide. Mpandowo unali ndi zogwirira ndi zosanjikapo manja uku ndi uku, ndiponso zifanizo ziŵiri za mikango iŵiri itaima pambali pa zosamizapo manjazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi ndi choyikapo mapazi cholumikizidwa ku mpandowo. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, ndi chifanizo cha mkango chitayima posanjikapo manjapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mpando wacifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi copondapo mapazi cagolidi, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.