2 Chronicles 9:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso mikango pa mbali zonse ziŵiri za kwerero lililonse, mikango khumi ndi iŵiri yonse pamodzi. Mpando sudapezekepo mu ufumu wina uliwonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mikango khumi ndi iwiri inaimirirapo, mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwe wotere m'ufumu uliwonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi imodzi aja. Umodzi mbali ina ya khwerero ndi wina mbali inayo. Palibe mpando wonga uwu umene unapangidwapo mu ufumu wina uliwonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mikango khumi ndi iwiri Inaimirirapo, mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwa wotere m'ufumu uli wonse.