2 Chronicles 9:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide, ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Siliva sanalinso kanthu pa nthaŵi ya Solomoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zipangizo zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali za golide woona; siliva sanayesedwe kanthu m'masiku a Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zikho zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndiponso zipangizo zonse za ku nyumba yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide oyengeka bwino. Panalibe chinthu chopangidwa ndi siliva, chifukwa siliva samayesedwa kanthu mʼnthawi ya Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zikho zomwera zonse za Solomo zinali zagolidi, ndi zipangizo zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali za golidi woona; siliva sanayesedwa kanthu m'masiku a Solomo.