2 Chronicles 9:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu inali ndi zombo zimene zinkapita ku Tarisisi ndi anyamata a mfumu Huramu, ndipo chaka chachitatu chilichonse, zombo za ku Tarisisi zinkabwera ndi golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golide, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inali ndi sitima zambiri zapamadzi zimene zimayendetsedwa ndi antchito a Hiramu. Zimabwera kamodzi pa zaka zitatu zilizonse zitanyamula golide, siliva ndi nyanga za njovu, ndiponso anyani ndi apusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golidi, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawanga mawanga.