2 Chronicles 9:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense mwa iwo ankabwera ndi mphatso zake, zinthu zasiliva ndi zagolide, zovala, zida zankhondo, zokometsera chakudya, akavalo ndi abulu. Ndipo zimenezi zinkachitika choncho chaka ndi chaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndi mure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka ndi chaka, aliyense amene amabwera, amabweretsa mphatso monga zipangizo zasiliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya komanso akavalo ndi abulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nabwera nao munthu yense mtulo wace, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolidi, zobvala, ndi zobvala za nkhondo, ndi zonunkhira, akavalo, ndi nyuru; momwemo caka ndi caka.