2 Chronicles 9:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina zonse za Solomoni kuyambira pa chiyambi mpaka kumaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la ulosi wa Ahiya wa ku Siloni, ndiponso m'buku lokamba zimene mneneri Ido adaziwona m'masomphenya zokhudza Yerobowamu mwana wa Nebati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ntchito zina zonse za Solomoni, kuyambira pachiyambi mpaka kumaliza, kodi sizinalembedwa mʼbuku la mbiri la mneneri Natani, ndi mʼbuku la uneneri wa Ahiya wa ku Silo ndi mʼbuku la masomphenya a mlosi Ido, lokamba za Yeroboamu mwana wa Nebati?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ena tsono a Solomo, oyamba ndi otsiriza, salembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobiamu mwana wa Nebati?