2 Chronicles 9:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide bambo wake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anamwalira nagona ndi makolo ake. Anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nagona Solomo pamodzi ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wace; ndipo Rehabiamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.