2 Chronicles 9:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndikuona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiuzeko zonse ngakhale ndi theka lomwe la nzeru zanu zonse. Mukupambana kutali mbiri imene ndidaaimva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sindinakhulupirira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sindinakhulupirire zimene ankanena mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe la kuchuluka kwa nzeru zanu, pakuti zaposa zimene ndinamva.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sindinakhulupira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zocuruka; mwa, onjezatu pa mbiri ndidaimva.