2 Chronicles 9:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando wake waufumu, kuti mukhale mfumu yotumikira Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adakulongani ufumu kuti muzilamulira Aisraele, chifukwa choti Mulungu wanu adakonda Israele mpaka muyaya, nafuna kuti akhalepo mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yake yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wacifumu wace, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ace; popeza Mulungu wanu anakonda Aisrayeli kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kucita ciweruzo ndi cilungamo.