2 Corinthians 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene timanyadira nchakuti mtima wathu umatichitira umboni kuti ponseponse pamene tidapita, koma makamakanso pakati panu, mayendedwe athu anali oyera ndi opanda chinyengo. Zinali choncho osati chifukwa chotsata nzeru za anthu ai, koma chifukwa Mulungu adatikomera mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa cikumbu mtima cathu, kuti m'ciyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'cisomo ca Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.