2 Corinthians 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndidaakonza ulendo wanga kuti ndidzere kwanu popita ku Masedoniya, ndi kuti ndidzerenso kwanu pochokera ku Masedoniyako. Ndinkafuna kuti potero mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga wopita ku Yudeya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo popyola kwanu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Makedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.