2 Corinthians 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi pamene ndidaaganiza kuchita zimenezi, inu mukuyesa kuti ndidaachita zinthu mwachibwana? Kaya zimene ndimaganiza kuzichita, kodi ndimangoziganiza mwaukapsala, kotero kuti ndingathe kunena kuti, “Inde, inde” ndiponso “Ai, ai” pa nthaŵi imodzi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo, pakufuna cimene, kodi ndinacitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?