2 Corinthians 1:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si kuti ticita ufumu pa cikhulupiriro canu, koma tikhala othandizana naco cimwemwe canu; pakuti ndi cikhulupiriro muimadi.