2 Corinthians 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati tikuzunzika, nkuti inu mupeze chokulimbitsani mtima ndiponso chipulumutso. Ngati ife atilimbitsa mtima, nkuti inunso mulimbitsidwe mtima ndi kulandira mphamvu za kupirira pamene mulikumva zoŵaŵa zomwezo zimene ifenso timamva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati tisautsidwa, kuli cifukwa ca citonthozo ndi cipulumutso canu; ngati titonthozedwa, kuli kwa citonthozo canu cimene cicititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.