2 Corinthians 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikhulupiriro chathu pa inu ncholimba. Tikudziŵa kuti monga mulikumva zoŵaŵa pamodzi nafe, momwemonso mudzapeza chokulimbitsani mtima pamodzi nafe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ciyembekezo cathu ca kwa inu ncokbazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi citonthozo.