2 Corinthians 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono abale, tifuna kuti mudziŵe, masautso amene tidakumana nawo ku dziko la Asiya, adatipsinja koopsa, kopitirira mphamvu zathu, kotero kuti sitinkayembekezanso kuti nkukhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za cisautso cathu tinakomana naco m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukuru, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;