2 Corinthians 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dzina la Yesu Khristu wa mtima woleza ndi wofatsa, ine Paulo mwiniwake, amene anthu ena amati ndine wamantha pamene ndili pamaso panu, koma wosaopa konse pamene ndili nanu kutali, ndikuti mundimve.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Kristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzicepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;