2 Corinthians 10:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sikuti timayesa kudzilinga kapena kudziyerekeza ndi ena amene amadzichitira okha umboni. Amapusa chabe pakungodziyesa ndi muyeso waowao, ndi kudzilinganiza ndi anzao a m'gulu lao lomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwookha, alibe nzeru.