2 Corinthians 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero sitinyadira ntchito zimene anthu ena adazigwira m'dera limene Mulungu adatiikira ife. Kwenikweni tikuyembekeza kuti chikhulupiriro chanu chidzakula, ndipo kuti ntchito yathunso pakati panu idzakula, koma osabzola malire a dera lathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
osadzitamandira popitirira muyeso mwa macititso a ena; koma tiri naco ciyembekezo kuti pakukula cikhulupiriro canu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa cilekezero cathu kwa kucurukira,