2 Corinthians 10:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kwanuko ndisadzakakamizidwe kudzudzula mosaopa konse anthu amene akuti machitidwe athu ndi otsata za anthu chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kumeneko ndisadzachite kuyankhula mwamphamvu monga mmene ndimayembekezera kudzachita kwa anthu ena amene amaganiza kuti machitidwe athu ndi ofanana ndi anthu a dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ndipempha kuti pokhala ndiri pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi,