2 Corinthians 10:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ganizani bwino pa zimene mukuwona ndi maso anu. Kodi pali wina amene amakhulupirira kuti ndi wake wa Khristu? Chabwino, koma akumbukire kuti monga iye ali wake wa Khristu, ifenso ndife ake a Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Kristu, ayesere icinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Kristu, koteronso ife.