2 Corinthians 11:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene ndikuchita tsopano, ndidzazichitabe, kuti ndisaŵapatse mpata onyenga aja amene akufuna danga loti anyadire, ndi kumanena kuti iwonso akugwira ntchito molingana ndi ife.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cimene ndicita, ndidzacitanso, kuti ndikawadulire cifukwa iwo akufuna cifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.