2 Corinthians 11:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nkuchita zotere. Tsopano ndilankhula ngati wopusa: zimene wina aliyense anganyadire, zomwezo inenso ndingathe kuzinyadira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi. Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.