2 Corinthians 11:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa maulendo anga ochuluka ndidakumana ndi zoopsa za mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa Ayuda anzanga, ndi zina zochokera kwa akunja. Ndidapeza zoopsa m'mizinda, m'thengo, ndi pakati pa abale onyenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mudzi, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
paulendo kawiri kawiri, moopsya mwace mwa mitsinje, moopsya mwace mwa olanda, 1 moopsya modzera kwa mtundu wanga, moopsya modzera kwa amitundu, moopsya m'mudzi, moopsya m'cipululu, moopsya m'nyanja, moopsya mwaabale onyenga;